T/A Chisemphere Yamwalira

Written by on February 28, 2018

Aku unduna wa za maboma aang’ono ndi chitukuko chakumidzi alengeza za imfa ya mfumu yaikulu Chisemphere ya m’boma la Kasungu.

Mfumu yaikulu Chisemphere, yomwe dzina lake ndi Petros Kumwenda yamwalira lamulungu pa 25 february, 2018 ku nyumba kwawo.

Mfumuyi inabadwa mchaka cha 1904, inakhazkitsidwa kukhala Sub T/A mchaka cha 1978 ndipo inakwezedwa kukhala T/A mchaka cha 2004.

Iwo asiya ana 15, zidzukulu 196 komanso zidzukulu tuzi zokwana 1760. Mwambo woyika m’manda thupi la T/A Chisemphere uchitika lachitatu likudzali pa 28 February, 2018 ku likulu lawo ku Khomawekha m’boma la Kasungu.


Radio Maria Malawi

Current track
TITLE
ARTIST