LAMULO LATSOPANO LOKHUDZA KACHIROMBO KA HIV KOMANSO MATENDA A AIDS PROG2

Alinafe Kunsamala

Mmwezi wa February chaka chino, boma linakhazikitsa lamulo latsopano lokhudza kachilombo ka HIV komaso matenda a Aids (HIV and Aids Prevention and Management Act).

Lawyer  Gabriel Chembezi akugawana nafe zambiri za lamulo latsopanoli maka pa mfundo izi:

1. Kodi lamulo limeneli lakhazikitsidwa chifukwa chani?

2. Kodi mukudziwa kuti ndi mulandu kusala munthu amene ali ndi HIV/Aids, kapena kuwulula kwa anthu ena pamene munthu wapezeka ndi HIV?

3. Kodi mukudziwa kuti ndi mulandu kwa olemba anthu ntchito kapena opereka maphunziro osiyanasiyana kukakamiza kuyeza munthu HIV asanamulembe ntchito kapena asanampatse malo a school?

4. Kodi mukudziwa kuti mutapezeka ndi HIV, lamuloli likupereka mphamvu kwa achipatala kuwulula zimenezi kwa mkazi wanu kapena mamuna wanu kapena wina aliyense amene mumakhala naye malo amodzi ndi cholinga choti mzanuyo atetezedwe?

5. Kodi mukudziwa kuti miyambo ya makolo monga kulowa kufa, chokolo, fisi ndi ina yomwe imathandizira kufalitsa kachilombo ka HIV ndiyoletsedwa ndipo ndi mulandu kupanga miyambo imeneyi?

Kondani kumvera Radio Maria Malawi nthawi zonse!
Kondani kuthandiza Radio Maria Malawi nthawi zonse!
Radio Maria Malawi, Liwu la Chikhritu mnyumba mwanu!!Current track

Title

Artist