Papa Apempha Achinyamata Akhale a Masomphenya

Written by on May 18, 2018

Mtsogoleri  wa mpingo wa katolika pa dziko lonse, Papa Francisco  wapempha achinyamata kuti azikhala ndi masomphenya komanso njira zothekera  kukwaniritsa maso mphenya awo.

Malipoti a wailesi ya Vatican ati Papa wanena izi pamene anayendera  achinyamata omwe ali mu bungwe la The Scholas Occurrentes ku Rome mdziko la Italy.

Bungweli linakhazikitsidwa ndi Papa Francisco   m`dziko la Argentina pamene anali Episikopi wa archidayosizi ya Buenos Aires ndipo pakadali pano bungweli likupezeka m`maiko  okwana 190.

M`mawu ake Papa walangiza achinyamata kuti  apitirize kukhala ndi maso mphenya mpaka zolinga zawo zitakwanilitsidwa.

Iye anapitiriza kunena kuti chikhulupiliro sichimakhumudwitsa  koma chimathandizira kulimba mtima, pakupita chitsogolo mpaka maloto onse atakwaniritsidwa.

Iye wauzanso achinyamata-wa kuti ali ndi kuthekera kochita bwino  ngati atakhala okhazikika mu zinthu zawo komanso kukhala ndi mtima  wothandiza ena, ndi cholinga choti miyoyo yawo ipite patsogolo.

Papa: Achinyamata akuyenera kukhala ndi masomphenya


Current track
Title
Artist