Blog

Aku unduna wa za maboma aang’ono ndi chitukuko chakumidzi alengeza za imfa ya mfumu yaikulu Chisemphere ya m’boma la Kasungu. Mfumu yaikulu Chisemphere, yomwe dzina lake ndi Petros Kumwenda yamwalira lamulungu pa 25 february, 2018 ku nyumba kwawo. Mfumuyi inabadwa mchaka cha 1904, inakhazkitsidwa kukhala Sub T/A mchaka cha 1978 ndipo inakwezedwa kukhala T/A mchaka […]

Bwalo loyamba la milandu m’boma la Ntchisi lalamula m’nyamata wina wa zaka 18 zakubadwa kuti akakhale ku ndende ya ana ya Kachere kwa zaka ziwiri kaamba kopezeka olakwa pa mulandu ogwilirira. Malinga ndi wofalitsa nkhani za apolisi m’bomalo Sergeant Gladson M`Bumpha, m’nyamatayu Petulo Simoni, pa 9 October chaka chatha anatengera ku nyumba kwake msungwana wina […]

Mpingo wa Anglican wayamikira m’tsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisko kaamba kokhudzidwa ndi mavuto akusowa kwa mtendere pakati pa anthu m’mayiko a South Sudan ndi Democratic Republic of Congo (DRC) omwe akudza kaamba ka nkhondo ndi mikangano yokhudza utsogoleri yomwe ikuchitika m’mayiko-wa. M’tsogoleri wa mpingowu Justin Webby ndi amene wanena izi kudzera […]

Ophunzira aku sukulu ya ukachenjede ya DMI-St. John The Baptist Universitym‘boma la Mangochiawapempha kuti asamatanganidwe ndi za m‘dziko kamba koti sizingawathandize pa moyo wawo. Bambo Ernest Mwinganyama, omwe amatumikira kuRadio Maria Malawi, anena izi pa msulo wa ophunzira pa sukulu-yi. Iwo ati ophunzira-wa ngati angamapewe zinthu zina zochitika m‘dzikoli, ndiye kuti zitha kuthandiza pa tsogolo […]


  • Pages

  • 1

Radio Maria Malawi

Current track
TITLE
ARTIST