Mpingo wa Anglican Uyamikira Papa Francisko

Written by on February 28, 2018

Mpingo wa Anglican wayamikira m’tsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisko kaamba kokhudzidwa ndi mavuto akusowa kwa mtendere pakati pa anthu m’mayiko a South Sudan ndi Democratic Republic of Congo (DRC) omwe akudza kaamba ka nkhondo ndi mikangano yokhudza utsogoleri yomwe ikuchitika m’mayiko-wa.

M’tsogoleri wa mpingowu Justin Webby ndi amene wanena izi kudzera mu uthenga wapadera umene mpingowu watulutsa.

Iye wati zomwe papa francisco anachita polimbikitsa mapemphero apadera opemphelera mtendere wa m’mayikowa pa 23 February ndi zinthu zotamandika ndipo zasonyeza chikondi chozama chomwe Papa Francisco ali nacho pakati pa anthu omwe akukomana ndi mavuto osiyanasiyana m’maikowa.


Continue reading

Radio Maria Malawi

Current track
TITLE
ARTIST