Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

Maofesi A Mkulu Woona Za Chitukuko Ndi Ntchito Zina Atsekedwa. 

 

Makhansala a m’boma la Zomba atseka ma ofesi a mkulu woyang’anira mapulani ndi ntchito za zitukuko komanso ofesi ya mkulu woyang’anira ntchito zosiyanasiyana za m’bomalo kaamba kosakondwa ndi momwe akulu-akulu awiri-wa akugwilira ntchito zawo.

 

Wapampando wa Boma la Zomba  Khansala Chikumbutso Likandawe wauza Radio Maria Malawi kuti aganiza zotseka maofesi-wa kaamba koti anthu awiri-wa akuwaganizira kuti akusakaza chuma cha khonsolo-yo.

Iwo ati zitukuko zambiri m’bomali sizikuoneka m’mene zikumathera ngakhale kuti ndalama zake zimakhala zitapelekedwa kale.

Koma poyankhulapo Bwana Mkubwa wa boma-li a Emmanuel  Bambe wati sanayembekedzere kuona zomwe zachitikazi kaamba koti sanalandire dandaulo lililonse kuchokera kwa makhansala-wa.

M’malo mwake a Bambe ati akhala pansi ndi makhansla-wo kuti amve madandaulo awo. Pakadali pano a Willard Chirwa omwe ndi mkulu woyang’anira mapulani ndi chitukuko komanso a Hestings Mulambuzi omwe ndi mkulu woyang’anira ntchito za boma-li awatumiza ku tchuthi mokakamiza.

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices