Ebola Yapha Anthu 23 Mdziko La DRC

Written by on May 18, 2018

Nthenda ya Ebola, akuti ikupitilirabe kufala mmadera osiyanasiyana m’dziko la Democratic Republic of Congo (DRC).

Malingana ndi malipoti a wailesi ya BBC, nduna ya za umoyo m’dzikomo yati pali mantha oti nthendayi itha kufika poipa kwambiri zomwe zingapangitse kuti pakhale povuta kuthana nayo.

Iyo yati m’dzinda wa Mbandaka ndi womwe uli ndi anthu oposera 1 miliyoni  omwe akhudzidwa ndi matenda-wa moti padakalipano anthu oposa 42 ndi omwe akhudzidwa ndi nthendayi, ndipo ena oposera 23 ndi omwe afa kamba ka matenda-wa.

M’modzi mwa akulu akulu ku bungwe loona za umoyo pa dziko lonse la World Health Organization (WHO) a Peter Salama, ati kubuka kwa nthendayi ndi chiopsezonso chachikulu maka kwa anthu a okhala m’mayiko omwe achita malire ndi dzikolo.


Current track

Title

Artist