Apempha Ophunzira Asatengeke ndi Zapadziko

Written by on February 28, 2018

Ophunzira aku sukulu ya ukachenjede ya DMI-St. John The Baptist Universitym‘boma la Mangochiawapempha kuti asamatanganidwe ndi za m‘dziko kamba koti sizingawathandize pa moyo wawo.

Bambo Ernest Mwinganyama, omwe amatumikira kuRadio Maria Malawi, anena izi pa msulo wa ophunzira pa sukulu-yi.

Iwo ati ophunzira-wa ngati angamapewe zinthu zina zochitika m‘dzikoli, ndiye kuti zitha kuthandiza pa tsogolo lawo mu zonse.

Polankhulanso ena mwa atsogoleri a bungwe la ophunzira achikatolika pa sukulu-yi Patrick Mambiandi Jane Chagundaayayamikira akuluakulu asukuluyi kamba kowalimbikitsa pa moyo wawo wa uzimu.

Pamenepa iwo ati ayetsetsa kuti azikumanakumana ndi kumalimbitsana pa zamoyo wawo wa uzimu ndi cholinga choti asataye chikhulupiliro ndi chiphunzitso cha mpingo wawo wa katolika.


Radio Maria Malawi

Current track
TITLE
ARTIST