Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

Anthu Asamalire Chilengedwe Pofuna Kupewa Njala 

 

Anthu mdziko muno ati akuyenera kutenga mbali yaikulu yoteteza chilengedwe pofuna kupewa vuto la kusowa kwa chakudya lomwe padakali pano lakhudza kwambiri dziko la Malawi.

Vicar General wa dayosizi ya Mangochi ya mpingo wakatolika Bambo Andrew Nkhata ndi omwe alankhula izi ku parishi ya St Loius ku Monkeybay mu dayosiziyi pa mwambo wokhazikitsa ntchito yogawa thandizo lomwe mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco anapereka ku dziko la Malawi kuti lithandize anthu omwe akhudzidwa ndi vuto la njala.

Iwo ati anthu ambiri akukumana ndi vuto la njala kamba kakusintha kwa nyengo kaamba koti anthu eni ake akulephera kusamala chilengedwe.

“Vuto la njala limene anthu ambiri akukumana nalo padakali pano ndi chifukwa choti anthu akulephera kusamala chilengedwe kaamba koti mbeu zikumakokoloka kaamba kodula mitengo mwa chisawawa,” anatero bambo Nkhata.

Polankhulapo mlembi wamkulu wa nthambi yoona za chitukuko mu mpingowu ya CADECOMmu dayosiziyi a Pietre Nthenda ati boma la dziko lino litalengeza kuti mdziko la Malawi muli njala, mpingo wakatolika kuno ku Malawi kudzera ku likulu lake ku Episcopal Conference of Malawi ECMunaganiza zopempha thandizo ku likulu la mpingo wakatolika pa dziko lonse.

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices