Amulamula Kukakhala ku Ndende ya Ana Kaamba Kogwililira

Written by on February 28, 2018

Bwalo loyamba la milandu m’boma la Ntchisi lalamula m’nyamata wina wa zaka 18 zakubadwa kuti akakhale ku ndende ya ana ya Kachere kwa zaka ziwiri kaamba kopezeka olakwa pa mulandu ogwilirira.

Malinga ndi wofalitsa nkhani za apolisi m’bomalo Sergeant Gladson M`Bumpha, m’nyamatayu Petulo Simoni, pa 9 October chaka chatha anatengera ku nyumba kwake msungwana wina wa zaka khumi ndi ziwiri (12) ndipo anagona naye kangapo konse ati ndi cholinga chomukwatira.

Makolo amsungwanayu atawona kusowa kwa mwana wawoyo anayamba kumufufuza ndipo anatsinidwa khutu ndi anthu ozungulira derali kuti akupezeka kunyumba kwa m’nyamatayu.

Makolo-wa anatengera nkhaniyi ku polisi ndipo mnyamatayu anauvomera mulanduwu.

Popereka chigamulo chake, First Grade Magistrate Dorothy Kalua anati mlanduwu ndi waukulu ndipo mnyamatayu amayenera kulandira chilango chokakhala ku ndende kuti anthu ena atengerepo phunziro.

Koma powona msinkhu wa myamatayu anamulamula kuti akhakhale ku malo osinthirako ana omwe amapalamula milandu yosiyanasiyana a Kachere Reformatory Centre kwa zaka ziwiri.

Petulo Simoni amachokera m’mudzi wa Thung’unda kwa mfumu yayikulu Chilooko m’boma lomwelo la Ntchisi. 


Radio Maria Malawi

Current track
TITLE
ARTIST