Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

Amai a Mpingo Wakatolika Athandiza Seminare Ya St Peter’s. 

 

Amai a bungwe la Catholic  Women Organization  (CWO)  m’dayosizi ya Zomba apereka katundu osiyanasiyana ku seminare yaikulu ya St Peter’s  m’bomalo.

 

Poyankhula ndi Radio Maria Malawi wapampando wa bungwe-li mu dayosizi-yi mai Elizabeth Meke wati bungwe lawo lipitiliza kuthandiza seminare-yi ndichlinga choti mpingo ukhale ndi ansembe ambiri.

 

Iwo ati akhristu ali ndi udindo wothandiza asemino-wa pa maphunziro ndinso umoyo wawo wa tsiku ndi tsiku kaamba koti nawonso ndi anthu ngati ife tomwe.

 

Ndipo Dikoni Charles Danken yemwe ndi mkulu woyang’anira a semino komanso madikoni pa seminare-yi wati ophunzira ku seminare-yi ndi osangalala kaamba koti anthu ambiri amawafunira zabwino pamene amawathandiza ndi zinthu zosiyanasiyana.

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices