Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

Zisankho Zapadera Zichitika Chaka Chino Chisanathe-MEC 

 

Bungwe lowona za chisankho mdziko muno la Malawi Electoral Commission (MEC) lati chisankho chapadera chomwe chalephereka chomwe chimayenera kuchitika m’madera ena a mdziko muno pa 6 June chichitika chaka chino chisanathe.

Mmodzi mwa akuluakulu ku bungweli Commissioner Clifford Baloyi ndi omwe anena izi poyankhapo madandaulo omwe anthu ena omwe ndi okhudzidwa ndi kuyimitsidwa kwa chisankhochi anapereka ku bungweli pamene limayenera kukhazikitsa ntchitoyi dzulo (lachinayi) pa Nathenje Teacher Development Centre, ku Lilongwe Msozi North constituency.

Iwo ati zisankhozi zayimitsidwa kaamba koti boma lanena kuti lilibe ndalama zoyendetsera zisankhozi ndipo ati ndalamazo zipezeka ndondomeko ya zachuma ya 2017/2018 ikakhazikitsidwa.

Padakali pano boma ati lapereka ndalama zokwana 187millionkwacha ku bungweli m’malo mwa ndalama zomwe zikufunika kuyendetsera chisankhochi zomwe ndi zokwana 501 million kwacha.

Chisankhochi chimayenera kuchitika m’madera a Msozi komwe ndi kumpoto kwa boma la Lilongwe, kum’mwera cha kumvuma kwa boma la Lilongwe, ward ya mtsiliza mdera la kuzambwe kwa mzinda wa Lilongwe komanso ku Mayani komwe ndi ku mpoto kwa boma la Dedza.

Padakali pano akuluakulu ena mdziko muno adzudzula bungwe la MEC kaamba kolephera kupereka uthenga woyenera wa kuyimitsidwa kwa chisankhochi mu nthawi yake monga momwenso zinachitikira pa chisankho chapadera chomwe chinachitika posachedwapa m’boma la Mchinji.

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices