Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

Papa Akhazikitsa Francisko Komanso Yasinta Kukhala Oyera pa 13 May 

 

Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisko walengeza kuti akhazikitsa ana awiri omwe anawonekeredwa ndi Amayi Maria ku Fatima, Francisko ndi Yasinta kukhala oyera pa 13 May pa ulendo wake womwe akayendere dziko la Portugal.

Malipoti a wailesi ya Vatican ati papa walengeza za kukwezedwa kwa anthu 35 omwe ambiri mwa iwo ndi amalitiri ochokera ku Latin America.

Pa mndandandawu ndi pomwenso patuluka mayina a Francisko ndi mchemwali wake  Yasinta Marto omwe pamodzi ndi msuweni wawo Lucia anawonekeredwa ndi Amayi Maria ku Fatima zaka 100 zapitazo.

Lucia yemwe anazakhala sisiteri anamwalira ali ndi zaka 98 pamene Francisko komanso Lucia anamwalira ali ndi zaka 9 komanso 11 kaamba ka nthenda ya chimfine.

Pa 13 May mchaka cha 2000 Papa Yohane Paulo Wachiwiri anatchula ana awiriwa kukhala odala.

Pakadali pano likulu la mpingo wa katolika ku Vatican likuwunika ngati Lucia ali woyenera kutchulidwa woyera.

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices