Contact us

P.O. Box 408,
Mangochi,
MALAWI.

Tel. (265) 01 599 608/627/602/617
Fax (265) 01 599 691
E-mail: radiomaria@africa-online.net

Papa Akumana ndi Pulezidenti wa Dziko la Lebanon 

 

Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco ati anachita zokambirana ndi mtsogoleri wa dziko la Lebanon Michel Aoun yemwe anakayendera likulu la mpingo wakatolikali.

Malinga ndi malipoti a wailesi ya Vatican pa mkumanowu atsogoleri awiriwa ati anakambirana za ubale wabwino umene ulipo pakati pa likulu la mpingo wakatolikali ndi dziko la Lebanon.

Papa anayamikira dziko la Lebanon kamba kolandira anthu othawa kwao ochokera mdziko la Syria komanso anawunikirana zina mwa njira zomwe angatsate pofuna kuthetsa kusamvana komwe kulipo mmaikowa.

Pomaliza Pulezidenti Aoun anakumana ndi mlembi wamkulu wa ku likulu la mpingowu Cardinal Pietro Parolin komansomlembi woona za maubale pakati pa mayiko Ambuye Paul Richard Gallagher.

 

On Air Studio Phone Numbers

Mobile App

Android devices
 
Apple devices
 
Windows Phone devices